Movatterモバイル変換


[0]ホーム

URL:


Jump to content
Wikipedia
Fufuzani

Afilika

From Wikipedia
(Redirected fromAfrica)
Afilika
Afilika

Afilika ndi chigawo chimodzi cha zigawo za pa dziko la pansi ndipo ndi chigawo cha chiwiri kwa madela lomwe kuli anthu ambiri, koma anthu ambiri ali kuAsia. Ku Africa kumakhala 14% ya anthu onse a pa dziko la pansi, chifukwa chiwelengelo cha anthu ku Afilika ku ndi 1 300miliyoni ( malinga ndi chiwelengelo cha anthu chomwe chinachitika mu 2013). Gawo la Afilika lili ndi mayiko 53, ndipo linazungulilidwa nsinyanja ya Mediterranean kumpoto,nyanja ya Red Sea kumpoto chakumvuma,nyanja ya Indian kummwera cha kumvuma ndinyanja ya Atlantic kuzambwe. Pali mayiko 46 a mu Africa ndi 53 kuphatikiza zilumba zonse.

Afilika, makamaka kumvuma kwa delari, kumatchuka kwambiri kuti ndi kumene anthu anachokera mtundu wa anthu ndipo anapezako zotsalira za anthu amene analipo zaka 7 miliyoni zapitazo.

Dera la Afilika lili mbali zonse ziwiri za mzere waEquator ndipo nyengo za mudelari zimasiyana siyana kumpoto ndi kummwera kwa mzerewu.

Kumene kunachokela dzinali

[Sinthani |sintha gwero]

Afili linali dzina la anthu amene ankakhala kumpoto kwa dela la Africa ku malo otchedwa Carthage. –Ca, amatanthauza anthu kapena malo.Anthu ena amaganiza kuti dzina loti Afilika linachokela ku:Liu lachilatini lakuti aprica limene limatanthauza malo owala dzuwa kwambiri

Liu lachigiriki aphrike limene limatanthauza malo amene sikumazizira.

Kakhalidwe ka malo ku derali

[Sinthani |sintha gwero]

Dziko lalikulu kwa mbiri kudera la Afilika ndi laSudan ndipo dziko lake laing‘ono kwambiri ndi laSeychelles lomwe ndi chilumba ku mmawa kwa delari. Dziko laling’ono pa gombe ndiGambia.

Munthu mozama pa nkhani za kakhalidwe ka dziko aPtolemy (85-165 AD) ndi amene anagawa Afilika kuchokela ku dera laAsia ndipo anasiyaNyanja yofiira ngati malire. Kulinso munthu wina dzina lakePearson Mpindi fatch ndi thug.

Nyengo, zachilengedwe ndi zomera

[Sinthani |sintha gwero]

Nyengo ku Afilika imayambira kukhala yotentha komanso yozizira kwambiri. Kumpoto kwa delari ndi kuchipululu ndi kotentha, pamene pakati ndi kummwera ndi kotentha komanso kuli nkhalango zowilira kwambiri. Pali Madela ena amene kuli nyengo zotentha kwambiri komanso zozizira kwambiri.

Kuchotsahttps://ny.wikipedia.org/w/index.php?title=Afilika&oldid=49749
Categories:

[8]ページ先頭

©2009-2025 Movatter.jp