Dziko la Malaŵilomwe kale linkatchulidwa kutiNyasaland, ndi dziko la demokilase lomwe lili ndi anthu ambiri ndipo lili cha ku m’mwera kwaAfrica. Dzikoli linayandikana ndiZambia cha ku m'madzulo,Tanzania cha ku mpoto ndiMozambique kuzungulira kum’mawa, kum'mwera ndi ku m'madzulo. Chiyambi cha dzina loti Malawi sichidziwika bwino bwino, koma anthu ofufuza amakhulupilira kuti dzinali linachokela kwa chilankhulo cha anthu a mu dzikoli a ku chigawo cha kum'mwera, ndipo limatanthauza “malawi wa moto”, koma mbendela ya dzikoli limatanthauza "kwacha" kunena kuti dzuwa lawala m'mamawa.Purezidenti wa Malawi
Mbiri
Anthu oyamba mu dziko la Malawi anali a chiKhoisan, amene ankachita ulenje komanso kutolela zakudya zomera zokha.Anthu a Chibantu anabwera ku dzikoli nthawi wakusamuka kwa anthu a chi Bantu. Dziko lomwe limatchulidwa kuti Malawi panoli ndi dera laMaravi, lomwe linakhazikitsidwa ndi anthu a Chichewa mu zaka za ku ma 1600. Achewa anali ochokera ku gulu la anthu lotchedwa ma Luba. Koyambilira ndi pakati pa zaka za mma 1900, anthu a Chizulu ochokela ku Ndandwe,KwaZulu-Natal mdziko laSouth Africa,omwe ali Angoni amene mfumu yawo inaliZwangendaba.
Dziko laBritain linalamulila mpaka chaka cha 1964, ngakhale anthu ena a Chimalawi anayeseysa kupeza ufulu wodzilamulira wokha. Mu zaka za m’ma 1950, nkhani yofuna ufulu wodzilamulira inakula, maka maka pamene dziko la Britain linakhazikitsaChitaganya chaRhodesia ndiNyasaland mu chaka cha 1953. Mu 1958,DokotalaHastings Kamuzu Banda anabwelera ku dzikoli atachokako kwa nthawi yaitali. Iyeyu anakhala mtsogoleli wa chipani chaNyasaland African Congress chomwe pambuyo chinasinthidwa dzina kukhalaMalawi Congress Party (MCP). Mu chaka cha 1959, Banda anamangidwa ndipo anatumizidwa kuGweruPrison mu dziko la Southern Rhodesia (lomwe pano limatchedwaZimbabwe chifukwa cha ndale zofuna kuti dzikoli lidzizilamulira lokha. Iyeyu anamasulidwa chaka cha 1960 pamene analoledwa kupita kuLondon mdziko laBritain kukatenga mbali pa msokhano wokambirana za malamulo.Pa 5 April 1961,chipani cha MCP chinapambana kuponsa zipani zonse pa chisankho chokhazikitsa ulamuliro wa tsopano. Ku msonkhano wokambirana za malamulo olamurira dziko ku London m’mwezi waNovembala mu chaka cha 1962, boma la Britain linabvomera kuti Nyasaland likhale dziko lodzilamulira pa lokha. Chisankho chimenechi chinathetsa chitaganya cha Rhodesia ndi Nyasaland, chifukha dziko la Nyasaland likanakhala lodziimira pa lokha. Banda ansankhidwa kukhalaPrime Minister pa 1Febuluale 1963 ngakhale boma la Britain linkalamulirabe nkhani za chuma, chitetezo komanso ulamuliro wa dzikoli. Malamulo a tsopano olamulira dziko anakhazikitsidwa m’mwezi waMeyi 1963, ndipo chitaganya chinathetsedwa pa 31Disembala 1963. Dziko la Malawi linapatsidwa ufulu woyima pa lokha pa 6Julaye 1964. Patapita zaka ziwili, dzikoli linakhalaLipabuliki lomwePulezidenti wake anali Dr. Banda ndipo analitchula kuti dziko lokhala ndi chipani chimodzi chokha. Mu 1970, Banda anapatsidwa u Pulezidenti wamuyaya wa MCP, ndipo 1971 anapatsidwa u Pulezidenti wa muyaya wa dziko la Malawi.
Chifukwa cha kukula kwa kusakhutilitsidwa ndi ulamuliro wa Dr Banda, ndiponso makalata wolembedwa ndi mipingo ndiponso zonena zamabungwe osakhala a boma, dziko la Malawi linapangitsaReferendamu yomwe anthu anafunsidwa boma lomwe iwo ankafuna. Pa 14 June 1993, anthu ochuluka a dzikoli anasankha kuti dzikoli likhale la zipani zambiri. Chisankho chinapangidwa pa 17 May 1994 ndipoBakili Muluzi amene anali mtsogoleli waUnited Democratic Front (UDF). Chipani cha UDF chinatenga mipando 82 mwa mipando 177 ya kuNyumba yolamulira boma ndipo chinakhazikitsa mgwirizano ndi chipani chaAlliance For Democracy (AFORD). Mgwirizanowu unathetsedwa m’chaka cka 1966 koma ena mwa anthu amene anali a AFORD anatsalilabe m’mboma.Malamulo olamulira dziko amene anakhazikitsidwa mu 1995 anathetsa mphamvu zomwe zinali za chipani cha MCP. Kufulumizitsakutsegula kwa malonda (economic libelarisation) ndi kukhonzatso kayendetsedwe ka zinthu m’dzikoli kunali mbali ya kusintha kwa ndale kwa dzikoli.
Kusankhanso kwa Pulezidenti wina mu ulamuliro wademokilase kunachitika mmwezi wa Meyi 2004 pamene woyimila UDF pa chisankhochi aDr. Bingu wa Muntharika anapambana pa chisanko chomwe aJohn Tembo woyimira MCP ndi aGwanda Chakuamba woyimiraMgwirizano Coalition, limene linali gulu lomwe a mipingo ndi azipani zina ankatsatira. Chifukwa chakampeni ndi dongosolo lomwe Bakili Muluzi anachita, chipani cha UDF chinankhazikitsa boma la zipani zambiri ndi zipani zina zotsutsa boma.